Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 5:25-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo munthu wamkazi amene anali ndi nthenda yacidwalire zaka khwni ndi ziwiri,

26. ndipo anamva zowawa zambiri ndi asing'anga ambiri, nalipira zonse anali nazo osacira pang'ono ponse, koma makamaka nthenda yace idakula,

27. m'mene iye anamva mbiri yace ya Yesu, anadza m'khamu kumbuyo kwace, nakhudza cobvala cace.

28. Pakuti ananena iye, Ngati ndikakhudza ngakhale zobvala zace ndidzapulumutsidwa.

29. Ndipo pomwepo kasupe wa nthenda yace adaphwa; ndipo anazindikira m'thupi kuti anaciritsidwa cibvutiko cace.

30. Ndipo pomwepo Yesu, pamene anazindikira mwa Iye yekha kuti mphamvu idaturuka mwa Iye, anapotoloka m'khamu, nanena, Ndani anakhudza zobvala zanga?

31. Ndipo ophunzira ace ananena kwa Iye, Muona kuti khamu lirikukanikiza Inu, ndipo munena kodi, Wandikhudza ndani?

32. Ndipo Iye anaunguza-unguza kumuona iye amene adacita ici,

33. Koma mkaziyo anacita mantha, ndi kunthunthumira, podziwa cimene anamcitira iye, nadza, namgwadira, namuuza coona conse.

34. Ndipo anati kwa iye, Mwana wamkaziwe, cikhulupiriro, cako cakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wocira cibvutiko cako.

35. M'mene iye ali cilankhulire, anafika a ku nyumba ya mkuru wa sunagoge, nanena, kuti, Mwana wako wafa; ubvutiranjinso Mphunzitsi?

36. Koma Yesu wosasamala mau olankhulidwawo, ananena kwa mkuru wa sunagoge, Usaope, khulupirira kokha.

37. Ndipo sanalola munthu yense kutsagana naye, koma Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wace wa Yakobo.

38. Ndipo anafika ku nyumba kwace kwa mkuru wa sunagoge; ndipo anaona cipiringu, ndi ocita maliro, ndi akukuwa ambiri

39. Ndipo m'mene atalowa, ananena nao, Mubuma ndi kulira bwanji? Mwana sanafa, koma ali m'tulo.

40. Ndipo anamseka Iye pwepwete, Koma Iye anawaturutsa onse, natenga atate wa mwana, ndi amace, ndi ajawo anali naye, nalowa m'mene munali mwanayo.

41. Ndipo anagwira dzanja lace la mwana, nanena kwa iye, Talita koumi; ndiko kunena posandulika, Buthu, ndinena ndi iwe, Uka.

42. Ndipo pomwepo buthulo linauka, niliyenda; pakuti linali la zaka khumi ndi ziwiri. Ndipo anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukuru.

Werengani mutu wathunthu Marko 5