Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 5:15-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wobvala ndi wa nzeru zace zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo.

16. Ndipo adapenyawo adawafotokozera umo anacitira ndi wogwidwa ziwandayo, ndi za nkhumbazo.

17. Ndipo anayamba kumpempha Iye kuti acoke m'malire ao,

18. Ndipo m'mene Iye analikulowa mungalawa, anampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye.

19. Ndipo sanamlola, koma ananena naye, Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikuru anakucitira Ambuye, ndi kuti anakucitira cifundo.

20. Ndipo anamuka nayamba kulalikira ku Dekapoli zinthu zazikuru Yesu adamcitira iye; ndipo anthu onse anazizwa.

21. Ndipo pamene Yesu anaolokanso mungalawa tsidya lina, khamu lalikuru linasonkhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja.

22. Ndipo anadzako mmodzi wa akuru a sunagoge, dzina lace Yairo; ndipo pakuona Iye, anagwada pa mapazi ace, nampempha kwambiri,

23. nanena, kuti, Kamwana kanga kabuthu kalimkutsirizika; ndikupemphani Inu mufikeko, muike manja anu pa iko, kuti kapulwnuke, ndi kukhala ndi moyo.

Werengani mutu wathunthu Marko 5