Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 5:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anafika tsidya lina la nyanja, ku dziko la Agerasa,

2. Ndipo pameneadaturuka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu woturuka kumanda wa mzimu wonyansa,

3. amene anayesa nyumba yace kumanda; ndipo palibe munthu anakhoza kummanganso, inde ngakhale ndi unyolo;

4. pakuti adafomangidwa kawiri kawiri ndi matangadza ndimaunyolo, ndipo anamwetula maunyolo, naduladula matangadza; ndipo palibe munthu anali ndi mphamvu yakumfuya.

5. Ndipo masiku onse, usiku ndi usana, anakhala m'manda ndi m'mapiri, napfuula, nadzitematema ndi miyala.

6. Ndipo pakuona Yesu kutali, anathamanga, namgwadira Iye;

7. ndipo anapfuula ndi mau olimba, nanena, Ndiri ndi ciani ine ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkurukuru? Ndikulumbirirani pa Mulungu, msandizunze.

8. Pakuti ananena kwa iye, Turuka iwe, mzimu wonyansa, kwa munthuyu.

9. Ndipo anamfunsa, Dzina lako ndani? Ndipo ananena kwa Iye, Dzina langa ndine Legio; cifukwa tiri ambiri.

10. Ndipo anampempha Iye kwambiri kuti asaiturutsire kunja kwace kwa dziko.

11. Ndipo panali pamenepo gulu lalikuru la nkhumba zirinkudya kuphiri.

12. Ndipo inampempha Iye, kuti, Titumizeni ife mu nkhumbazo, kuti tilowe mu izo.

13. Ndipo anailolao Ndipo mizimu yonyansa inaturuka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m'nyanja.

Werengani mutu wathunthu Marko 5