Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 4:9-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo ananena, Amene ali nao makutu akumva amve.

10. Ndipo pamene anakhala pa yekha, iwo amene anali pafupi ndi Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo anamfunsa za mafanizo.

11. Ndipo Iye ananena nao, Kwa inu kwapatsidwa cinsinsi ca Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonse zicitidwa m'mafanizo;

12. kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa.

13. Ndipo ananena nao, Simudziwa kodi fanizo ili? mukazindikira bwanji mafanizo onse?

14. Wofesa afesa mau.

15. Ndipo iwo ndiwo a m'mbali mwa njira mofesedwamo mau; ndipo pamene anamva, pomwepo akudza Satana nacotsa mau ofesedwa mwa iwo.

16. Ndipo momwemonso iwo ndiwo amene afesedwa pathanthwe, atamva mau, awalandira pomwepo ndi kusekera;

17. ndipo alibe mizu mwa iwo okha, koma akhala kanthawi; pamenepo pakudza masautso kapena mazunzo cifukwa ca mau, pomwepo akhumudwa.

18. Ndipo ena ndiwo akufesedwa kuminga; iwo ndiwo amene adamva mau,

19. ndipo malabadiro a dziko lapansi, ndi cinyengo ca cuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mau, ndipo akhala opanda cipatso.

Werengani mutu wathunthu Marko 4