Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 4:36-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Ndipo posiya khamulo anamtenga apite nao, monga momwe anali, mungalawa. Ndipo panali ngalawa zina pamodzi ndi Iye.

37. Ndipo panauka namondwe wamkuru wa mphepo, ndi mafunde angabvira mungalawa, motero kuti ngalawa inayamba kudzala.

38. Ndipo Iye mwini anali kutsigiro, nagona tulo pamtsamiro; ndipo anamuutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti titayika ife?

39. Ndipo anauka, nadzudzula mphepo, nati kwa nyanja, kuti, Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo inaleka, ndipokunagwa bata lalikuru.

40. Ndipo ananena nao, Mucitiranji mantha? kufikira tsopano mulibe cikhulupiriro kodi?

41. Ndipo iwo anacita mantha akuru, nanenana wina ndi mnzace, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?

Werengani mutu wathunthu Marko 4