Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 4:29-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Pakucha zipatso, pamenepo atumiza zenga, pakuti nthawi yakumweta yafika.

30. Ndipo ananena, Tidzafaniziranji Ufumu wa Mulungu? kapena tidzaulinganiza ndi fanizo lotani?

31. Ngati mbeu yampiru, imene ikafesedwapanthaka, ingakhale icepa ndi mbeu zonse za padziko,

32. koma pamene ifesedwa, imera nikula koposa zitsamba zonse, nicita nthambi zazikuru; kotero kuti mbalame za m'mlengalenga zikhoza kubindikira mumthunzi mwace.

33. Ndipo ndi mafanizo otere ambiri analankhula nao mau, 1 monga anakhoza kumva;

34. ndipo sanalankhula nao wopanda fanizo: koma m'tseri anatanthauzira zonse kwa ophunzira ace.

35. Ndipo dzuwa lomwelo, pofika madzulo, ananena kwa iwo, Tiolokere tsidya lina.

36. Ndipo posiya khamulo anamtenga apite nao, monga momwe anali, mungalawa. Ndipo panali ngalawa zina pamodzi ndi Iye.

37. Ndipo panauka namondwe wamkuru wa mphepo, ndi mafunde angabvira mungalawa, motero kuti ngalawa inayamba kudzala.

38. Ndipo Iye mwini anali kutsigiro, nagona tulo pamtsamiro; ndipo anamuutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti titayika ife?

39. Ndipo anauka, nadzudzula mphepo, nati kwa nyanja, kuti, Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo inaleka, ndipokunagwa bata lalikuru.

40. Ndipo ananena nao, Mucitiranji mantha? kufikira tsopano mulibe cikhulupiriro kodi?

41. Ndipo iwo anacita mantha akuru, nanenana wina ndi mnzace, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?

Werengani mutu wathunthu Marko 4