Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 4:18-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo ena ndiwo akufesedwa kuminga; iwo ndiwo amene adamva mau,

19. ndipo malabadiro a dziko lapansi, ndi cinyengo ca cuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mau, ndipo akhala opanda cipatso.

20. Ndipo iwo ofesedwa pa nthaka yabwino ndiwo oterewa akumva mau, nawalandira, nabala zipatso zakupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi.

21. Ndipo ananena ndi iwo, Kodi atenga nyali kuti akaibvundikire mbiya, kapena akaiike pansi pa kama, osati kuti akaiike pa coikapo cace?

22. Pakuti kulibe kanthu kobisika, koma kuti kaonetsedwe; kapena kulibe kanthu kanakhala kam'tseri, koma kuti kakaululidwe.

23. Ngati munthu ali nao makutu akumva, amve.

24. Ndipo ananena nao, Yang'anirani cimene mukumva; ndi muyeso umene muyesera nao udzayesedwa kwa inu; ndipo kudzaonjezedwa kwa inu.

25. Pakuti kwa iye amene ali nako kanthu, kadzapatsidwa; ndipo kwa iye amene alibe kanthu, kadzacotsedwa ngakhale kanthu kali konse ali nako.

26. Ndipo ananena, Ufumu wa Mulungu uli wotero, monga ngati munthu akataya mbeu panthaka;

27. nakagona ndi kuuka, usiku ndi usana, ndipo mbeu zikamera, ndi kukula, iye sadziwa umo zicitira.

28. Nthaka ibala zipatso zace yokha; uyamba mmera, zitsata ngala, pamenepo maso okhwima m'ngalamo.

29. Pakucha zipatso, pamenepo atumiza zenga, pakuti nthawi yakumweta yafika.

30. Ndipo ananena, Tidzafaniziranji Ufumu wa Mulungu? kapena tidzaulinganiza ndi fanizo lotani?

31. Ngati mbeu yampiru, imene ikafesedwapanthaka, ingakhale icepa ndi mbeu zonse za padziko,

32. koma pamene ifesedwa, imera nikula koposa zitsamba zonse, nicita nthambi zazikuru; kotero kuti mbalame za m'mlengalenga zikhoza kubindikira mumthunzi mwace.

Werengani mutu wathunthu Marko 4