Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 4:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja, Ndipo anasonkhana kwa Iye khamu lalikurukuru, kotero kuti analowa Iye mungalawa, nakhala m'nyanja; ndipo khamu lonse linakhala pamtunda m'mbali mwa nyanja.

2. Ndipo anawaphunzitsa zinthu zambiri m'mafanizo, nanena nao m'ciphunzitso cace,

3. Mverani: taonani, wofesa anaturuka kukafesa;

4. ndipo kunali, m'kufesa kwace, zina zinagwa m'mbali mwanjira, ndi mbalamezinadza ndi kuzitha kudya,

5. Ndipo zina zinagwa pa nthaka yathanthwe, pamene panalibe nthaka yambiri; ndipo pomwepo zinamera, cifukwa zinalibe nthaka yakuya;

6. ndipo litakwera dzuwa zinapserera; ndipo popeza zinalibe mizu zinakhwinyata.

7. Ndipo zina zinagwa paminga, ndipominga inakula, nizitsamwitsa, ndipo sizinabala zipatso.

8. Ndipo zina zinagwa m'nthaka yabwino, ndipo zinapatsa zipatso, ndi kukula ndi kucuruka; ndipo zinabala kupindula makumi atatu, ndi makumi asanundi limodzi, ndi makumi khumi.

9. Ndipo ananena, Amene ali nao makutu akumva amve.

Werengani mutu wathunthu Marko 4