1. Ndipo anayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja, Ndipo anasonkhana kwa Iye khamu lalikurukuru, kotero kuti analowa Iye mungalawa, nakhala m'nyanja; ndipo khamu lonse linakhala pamtunda m'mbali mwa nyanja.
2. Ndipo anawaphunzitsa zinthu zambiri m'mafanizo, nanena nao m'ciphunzitso cace,
3. Mverani: taonani, wofesa anaturuka kukafesa;
4. ndipo kunali, m'kufesa kwace, zina zinagwa m'mbali mwanjira, ndi mbalamezinadza ndi kuzitha kudya,
5. Ndipo zina zinagwa pa nthaka yathanthwe, pamene panalibe nthaka yambiri; ndipo pomwepo zinamera, cifukwa zinalibe nthaka yakuya;
6. ndipo litakwera dzuwa zinapserera; ndipo popeza zinalibe mizu zinakhwinyata.
7. Ndipo zina zinagwa paminga, ndipominga inakula, nizitsamwitsa, ndipo sizinabala zipatso.