Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 3:4-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa dzuwa la Sabata kucita zabwino, kapena zoipa? kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala cete.

5. Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva cisoni cifukwa ca kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linacira dzanja lace.

6. Ndipo Afarisi anaturuka, ndipo pomwepo anamkhalira upo ndi Aherode, wakumuononga Iye.

7. Ndipo Yesu anacokako pamodzi ndi ophunzira ace nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikuru la a ku Galileya, ndi aku Yudeya,

8. ndi a ku Yerusalemu, ndi a ku Idumeya, ndi a ku tsidya lina la Y ordano, ndi a kufupi ku Turo ndi Sidoni, khamu lalikuru, pakumva zazikuruzo anazicita, linadza kwa Iye.

9. Ndipo anati kwa ophunzira ace, kuti kangalawa kamlinde Iye, cifukwa ca khamulo, kuti angamkanikize Iye,

10. pakuti adawaciritsa ambiri; kotero kuti onse akukhala nazo zowawa anakanikiza Iye, kuti akamkhudze.

11. Ndipo mizimu yonyansa, m'mene inamuona Iye, inamgwadira, nipfuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.

12. Ndipo anailimbitsira mau kuti isamuulule Iye.

13. Ndipo anakwera m'phiri, nadziitanira iwo amene anawafuna Iye mwini; ndipo anadza kwa Iye.

14. Ndipo anaika khumi ndi awiri, kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kulalikira,

Werengani mutu wathunthu Marko 3