Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 3:27-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Komatu palibe munthu akhoza kulowa m'nvumba ya mwini mphamvu, ndi kufunkha akatundu ace, koma athange wamanga mwini mphamvuyo; ndipo pamenepo adzafunkha za m'nyumba mwace.

28. Indetu, ndinena ndi inu, Adzakhululukidwa macimo onse a ana a anthu, ndi zamwano ziri zonse adzacita mwano nazo;

29. koma ali yense adzacitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anaparamuladi cimo losatha;

30. pakuti adanena, Ali ndi mzimu wonyansa.

31. Ndipo anadza amace ndi abale ace; naima kunja, namtumira uthenga kumuitana.

32. Ndipo anthu ambiri anakhala pansi pomzinga; nanena kwa Iye, Onani, amanu ndi abale anu ali kunja akufunani Inu.

33. Ndipo anawayankha nanena, Amai wanga ndi abale anga ndani?

34. Ndipo anawaunguza-unguza iwo akumzingawo, nanena, Taonani, amai wanga ndi abale anga.

35. Pakuti ali yense acita cifuniro ca Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo, ndi amai.

Werengani mutu wathunthu Marko 3