Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 3:25-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo nyumba ikagawanika pa iyo yokha, siikhoza kukhazikika nyumbayo,

26. Ndipo Satana akadziukira mwini yekha, nagawanika, sakhoza kukhazikika, koma atsirizika.

27. Komatu palibe munthu akhoza kulowa m'nvumba ya mwini mphamvu, ndi kufunkha akatundu ace, koma athange wamanga mwini mphamvuyo; ndipo pamenepo adzafunkha za m'nyumba mwace.

28. Indetu, ndinena ndi inu, Adzakhululukidwa macimo onse a ana a anthu, ndi zamwano ziri zonse adzacita mwano nazo;

29. koma ali yense adzacitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anaparamuladi cimo losatha;

30. pakuti adanena, Ali ndi mzimu wonyansa.

31. Ndipo anadza amace ndi abale ace; naima kunja, namtumira uthenga kumuitana.

32. Ndipo anthu ambiri anakhala pansi pomzinga; nanena kwa Iye, Onani, amanu ndi abale anu ali kunja akufunani Inu.

33. Ndipo anawayankha nanena, Amai wanga ndi abale anga ndani?

34. Ndipo anawaunguza-unguza iwo akumzingawo, nanena, Taonani, amai wanga ndi abale anga.

35. Pakuti ali yense acita cifuniro ca Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo, ndi amai.

Werengani mutu wathunthu Marko 3