Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 3:11-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo mizimu yonyansa, m'mene inamuona Iye, inamgwadira, nipfuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.

12. Ndipo anailimbitsira mau kuti isamuulule Iye.

13. Ndipo anakwera m'phiri, nadziitanira iwo amene anawafuna Iye mwini; ndipo anadza kwa Iye.

14. Ndipo anaika khumi ndi awiri, kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kulalikira,

15. ndi kuti akhale nao ulamuliro wakuturutsa ziwanda.

16. Ndipo Simoni anamucha Petro;

17. ndi Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace wa Yakobo, iwo anawacha Boanerge, ndiko kuti, Ana a bingu;

18. ndi Andreya, ndi Filipo, ndi Bartolomeyo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani,

19. ndi Yudase Isikariote, ndiye amene anampereka Iye.Ndipo analowa m'nyumba.

20. Ndipo anthu ambiri anasonkhananso, kotero kuti sanathe iwo konse kudya.

21. Ndipo pamene abale ace anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaruka.

22. Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Beelzibule, ndipo, Ndi mkuru wao wa ziwanda aturutsa ziwanda.

23. Ndipo m'mene adawaitana iwo, ananena nao m'mafanizo, Satana angathe bwanji kuturutsa Satana?

24. Ndipo ufumu ukagawanika pa uwu wokha, sukhoza kukhazikika.

Werengani mutu wathunthu Marko 3