Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 16:17-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo zizindikilo izi zidzawatsata iwo akukhulupirira; m'dzina langa adzaturutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;

18. adzatola njoka, ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzaika manja ao pa odwala, ndipo adzacira.

19. Pamenepo Ambuye Yesu, ata-tha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala pa dzanja lamanja la Mulungu.

20. Ndipo iwowa anaturuka, nalalikira ponse ponse, ndipo Ambuye anacita nao pamodzi, natsimikiza mau ndi zizindikilo zakutsatapo, Amen.

Werengani mutu wathunthu Marko 16