Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 16:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo litapita Sabata, Maliya wa Magadala, ndi Maliya amace wa Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira, kuti akadze kumdzoza Iye.

2. Ndipo anadza kumanda mamawa tsiku loyamba la Sabata, litaturuka dzuwa.

3. Ndipo analikunena mwa okha, Adzatikunkhunizira ndam mwalawo, pa khomo la manda?

4. Ndipo pamene anakweza maso anaona kuti mwala wakunkhunizidwa pakuti unali waukuru ndithu.

Werengani mutu wathunthu Marko 16