Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 15:40-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

40. Ndipo analinso kumeneko akazi akuyang'anira kutali; mwa iwo anali Maliya wa Magadala, ndi Maliya amace wa Yakobo wamng'ono ndi wa Yose, ndi Salome;

41. amene anamtsata Iye, pamene anali m'Galileya, namtumikira; ndi akazi ena ambiri, amene anakwera kudza ndi Iye ku Yerusalemu.

42. Ndipo atafika tsono madzulo, popeza mpa tsiku lokonzera, ndilo la pambuyo pa Sabata,

43. anadzapo Y osefe wa ku Arimateya, mkulu wa mirandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wace wa Yesu.

Werengani mutu wathunthu Marko 15