Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 15:30-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. udzipulumutse mwini, nutsike pamtanda.

31. Moteronso ansembe akuru anamtonza mwa iwo okha pamodzi ndi alembi, nanena, Anapulumutsa ena; sakhoza kudzipulumutsa yekha.

32. Atsike tsopano pamtanda, Kristu Mfumu ya Israyeli, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupacikidwa naye anamlalatira.

33. Ndipo pofika ora lacisanu ndi cimodzi, panali mdima pa dziko lonse, kufikira ora lacisanu ndi cinai.

34. Ndipo pa ora lacisanu ndi cinai Yesu anapfuula ndi mau okweza, Eloi, Eloi, lama sabakitani? ndiko kusandulika,Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?

35. Ndipo ena akuimirirapo, paku mva, ananena, Taonani, aitana Eliya

36. Ndipo anathamanga wina, nadzaza cinkhupule ndi vinyo wosasa naciika pabango, namwetsa Iye nanena, Lekani; tione ngati Eliys adza kudzamtsitsa.

37. Ndipo Yesr anaturutsa mau okweza, napereka mzimu wace.

38. Ndipo cinsart cocinga ca m'Kacisi cinang'ambika pakati, kuyambira kumwamba kufikira pansi.

39. Ndipo pamene kenturiyo, woimirirapo popenyana ndi Iye, anaona kuti anapereka mzimu kotero, anati, Zoonadi, munthu uyu anali Mwana wa Mulungu.

40. Ndipo analinso kumeneko akazi akuyang'anira kutali; mwa iwo anali Maliya wa Magadala, ndi Maliya amace wa Yakobo wamng'ono ndi wa Yose, ndi Salome;

41. amene anamtsata Iye, pamene anali m'Galileya, namtumikira; ndi akazi ena ambiri, amene anakwera kudza ndi Iye ku Yerusalemu.

42. Ndipo atafika tsono madzulo, popeza mpa tsiku lokonzera, ndilo la pambuyo pa Sabata,

Werengani mutu wathunthu Marko 15