Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 15:26-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo lembo la mlandu wace linalembedwa pamwamba, MFUMU YAAYUDA.

27. Ndipo anapacika pamodzi ndi Iye acifwamba awiri; mmodzi ku dzanja lace lamanja ndi wina kulamanzere.[

28. ]

29. Ndipo iwo akupitirirapo anamcitira mwano, napukusa mitu yao, nanena, Ha! iwe wakupasula Kacisi, ndi kummanga masiku atatu,

30. udzipulumutse mwini, nutsike pamtanda.

31. Moteronso ansembe akuru anamtonza mwa iwo okha pamodzi ndi alembi, nanena, Anapulumutsa ena; sakhoza kudzipulumutsa yekha.

32. Atsike tsopano pamtanda, Kristu Mfumu ya Israyeli, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupacikidwa naye anamlalatira.

33. Ndipo pofika ora lacisanu ndi cimodzi, panali mdima pa dziko lonse, kufikira ora lacisanu ndi cinai.

34. Ndipo pa ora lacisanu ndi cinai Yesu anapfuula ndi mau okweza, Eloi, Eloi, lama sabakitani? ndiko kusandulika,Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?

35. Ndipo ena akuimirirapo, paku mva, ananena, Taonani, aitana Eliya

Werengani mutu wathunthu Marko 15