Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 15:10-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pakuti anazindikira kuti ansembe akuru anampereka Iye mwanjiru.

11. Koma ansembe akuru anasonkezera khamulo, kuti makamaka awamasulire Baraba.

12. Ndipo Pilato anawayankhanso, nati kwa iwo, Pamenepo ndidzacita ciani ndi Iye amene mumchula Mfumu ya Ayuda?

13. Ndipo anapfuulanso, Mpacikeni pamtanda.

14. Ndipo Pilato ananena nao, Pakuti Iye anacita coipa cotani? Koma iwo anapfuulitsatu, Mpacikeni Iye.

15. Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Baraba, napereka Yesu, atamkwapula, akampacike pamtanda.

16. Ndipo asilikari anacoka naye nalowa m'bwalo, ndilo Pretorio; nasonkhanitsa gulu lao lonse.

17. Ndipo anambveka Iye cibakuwa, naluka korona waminga, nambveka pa Iye;

18. ndipo anayamba kumlankhula Iye, kuti, Tikuoneni, Mfumu ya Ayuda!

19. Ndipo anampanda Iye pamutu pace ndi bango, namthira malobvu, nampindira maondo, namlambira.

20. Ndipo atatha kumnyoza anambvula cibakuwaco nambveka Iye zobvala zace. Ndipo anaturuka naye kuti akampacike Iye pamtanda.

21. Ndipo anakangamiza wina wopitirirapo, Simoni wa ku Kurene, alikucokera kuminda, atate wao wa Alesandere ndi Rufu, kuti anyamule mtanda wace.

22. Ndipo anamtenga kunka naye ku malo Golgota, ndiwo, osandulika, Malo-a-bade.

23. Ndipo anampatsa vinyo wosanganiza ndi mure; koma Iye sanamlandira.

24. Ndipo anampacika Iye, nagawana zobvala zace mwa iwo okha, ndi kucita maere pa izo, kuti adziwe yense adzatengaciani.

Werengani mutu wathunthu Marko 15