Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 15:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe akuru, ndi akuru a anthu, ndi alembi, ndi akuru a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato.

2. Ndipo Pilato anamfunsa Iye, Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda? Ndipo anayankha, nanena naye, Mwatero.

3. Ndipo ansembe akuru anamnenera Iye zinthu zambiri.

4. Ndipo Pilato anamfunsanso, nanena, Suyankha kanthu kodi? taona, akunenera Iwe zinthu zambiri zotere.

5. Koma Yesu sanayankhanso kanthu; kotero kuti Pilato anazizwa.

6. Ndipo adafuwamasulira paphwando wandende mmodzi, amene iwo anampempha,

7. Ndipo analipo wina dzina lace Baraba, womangidwa pamodzi ndi opanduka, amene anapha munthu mumphandumo.

8. Ndipo khamu la anthu anabwera nayamba kupempha kuti acite monga adafuwacitira.

9. Ndipo Pilato anawayankha, nanena nao, Kodi mufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayuda?

10. Pakuti anazindikira kuti ansembe akuru anampereka Iye mwanjiru.

11. Koma ansembe akuru anasonkezera khamulo, kuti makamaka awamasulire Baraba.

12. Ndipo Pilato anawayankhanso, nati kwa iwo, Pamenepo ndidzacita ciani ndi Iye amene mumchula Mfumu ya Ayuda?

13. Ndipo anapfuulanso, Mpacikeni pamtanda.

14. Ndipo Pilato ananena nao, Pakuti Iye anacita coipa cotani? Koma iwo anapfuulitsatu, Mpacikeni Iye.

15. Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Baraba, napereka Yesu, atamkwapula, akampacike pamtanda.

16. Ndipo asilikari anacoka naye nalowa m'bwalo, ndilo Pretorio; nasonkhanitsa gulu lao lonse.

Werengani mutu wathunthu Marko 15