Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 14:53-63 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

53. Ndipo ananka naye Yesu kwa mkulu wa ansembe; ndipo anasonkhana kwa iye ansembe akuru onse ndi akuru a anthu, ndi alembi,

54. Ndipo Petro adamtsata Iye kutali, kufikira kulowa m'bwalo la mkulu wa ansembe; ndipo anali kukhala pansi pamodzi ndi anyamata, ndi kuotha moto.

55. Ndipo ansembe akuru ndi akuru a milandu onse anafunafuna umboni wakutsutsa nao Yesu kuti amuphe Iye; koma sanaupeza.

56. Pakuti ambiri anamcitira umboni wonama, ndipo umboni wao sunalingana.

57. Ndipo ananyamukapo ena, namcitira umboni wakunama, nanena kuti,

58. Ife tinamva Iye alikunena, kuti, Ine ndidzaononga Kacisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja.

59. Ndipo ngakhale momwemo umboni wao sunalingana.

60. Ndipo mkulu wa ansembe ananyamuka pakati, namfunsa Yesu, nanena, Suyankha kanthu kodi? Nciani ici cimene awa alikucitira mboni?

61. Koma anakhala cete, osayankhakanthu. Mkulu wa ansembe anamfunsanso, nanena naye, Kodi Iwe ndiwe Kristu, Mwana wace wa Wolemekezeka?

62. Ndipo Yesu anati, Ndine amene; ndipo mudzaona Mwana wa munthu alikukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo ya kumwamba.

63. Ndipo mkulu wa ansembe anang'amba maraya ace, nanena, Tifuniranjinso mboni zina?

Werengani mutu wathunthu Marko 14