Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 14:31-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Koma iye analimbitsa mau cilimbitsire, kuti, Ngakhale ndidzafa nanu, sindidzakana Inu. Ndipo onsewo anatero.

32. Ndipo iwo anadza ku malo dzina lace Getsemane; ndipo ananena kwa ophunzira ace, Bakhalani pano, kufikira ndikapemphera.

33. Ndipo anatenga pamodzi ndi Iye Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nayamba kudabwa kwambiri, ndi kusauka mtima ndithu.

34. Ndipo ananena nao, Moyo wanga uli wa cisoni cambiri, kufikira imfa. Bakhalani pano, nimudikire.

35. Ndipo Iye anapita m'tsogolo pang'ono, nagwa pansi, napemphera kuti ngati nkutheka nthawi imene impitirire.

36. Ndipo ananena, Abba, Atate, zinthu zonse zitheka ndi Inu; mundicotsere cikho ici; komatu si cimene ndifuna Ine, koma cimene mufuna Inu.

37. Ndipo anadza nawapeza iwo ali m'tulo, nanena ndi Petro, Simoni, ugona kodi? unalibe mphamvu yakudikira ora limodzi kodi?

38. Dikirani, pempherani, kuti mungalowe m'kuyesedwa; mzimutu uli wakufuna, koma thupi liri lolefuka.

39. Ndipo anacokanso, napemphera, nanena mau omwewo.

40. Ndipo anadzanso nawapeza ali m'tulo, pakuti maso ao analemeradi; ndipo sanadziwa comyankha Iye.

Werengani mutu wathunthu Marko 14