Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 14:21-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Pakuti Mwana wa munthu amukadi, monga kwalembedwa za Iye; koma tsoka munthuyo amene apereka Mwana wa munthu! Kukadakhala bwino kwa munthu ameneyo ngati sakadabadwa iye.

22. Ndipo pamene iwo analikudya, Iye anatenga mkate, ndipo pamene anadalitsa, ananyema, napereka kwa iwo, kuti, Tengani; thupi langa ndi ili.

23. Ndipo anatenga cikho, ndipo pamene adayamika, anapereka kwa iwo; ndipo iwo onse anamweramo.

24. Ndipo Iye anati kwa iwo, ici ndi mwazi wanga wa cipangano, wothiridwa cifukwa ca anthu ambiri.

25. Ndithu ndinena nanu, Sindidzamwanso cipatso ca mpesa, kufikira tsiku lijalo, limene ndidzamwa ico catsopano mu Ufumu wa Mulungu.

26. Ndipo atayimba nyimbo, anaturuka, namuka ku phiri la Azitona.

27. Ndipo Yesu ananena nao, Mudzakhumudwa nonsenu; pakuti kwalembedwa,Ndidzakantha mbusa, ndi nkhosa zidzamwazika.

28. Komatu nditadzauka ndidzatsogolera inu ku Galileya.

29. Koma Petro ananena naye, Angakhale adzakhumudwa onse, komatu ine iai.

30. Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu.

31. Koma iye analimbitsa mau cilimbitsire, kuti, Ngakhale ndidzafa nanu, sindidzakana Inu. Ndipo onsewo anatero.

Werengani mutu wathunthu Marko 14