Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 14:11-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo pamene iwo anamva, anasekera, nalonjezana naye kuti adzampatsa ndalama. Ndipo iye anafunafuna pompereka Iye bwino.

12. Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda cotupitsa, pamene amapha Paskha, ophunzira ace ananena naye, Mufuna tinke kuti, tikakonze mkadyereko Paskha?

13. Ndipo anatuma awiri a ophunzira ace, nanena nao, Lowani m'mzinda, ndipo adzakomana nanu munthu wakusenza mtsuko wa madzi; mumtsate iye;

14. ndipo kumene akalowako iye, munene naye mwini nyumba, Mphunzitsi anena, Ciri kuti cipinda ca alendo canga, m'menemo ndikadye Paskha ndi ophunzira anga?

15. Ndipo iye yekha adzakusonyezani cipinda ca pamwamba cacikuru coyalamo ndi cokonzedwa; ndipo m'menemo mutikonzere.

16. Ndipo ophunzira anaturuka, nafika m'mzinda, napeza monga anati kwa iwo; ndipo anakonza Paskha.

17. Ndipo pofika madzulo anadza Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.

18. Ndipo pamene anaseama iwo kudya, Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Mmodzi wa inu adzandipereka Ine, ndiye wakudya ndi Ine pamodzi.

19. Anayamba iwo kukhala ndi cisoni, ndi kunena naye mmodzi mmodzi, kuti, Ndine kodi?

20. Ndipo anati kwa iwo, Mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndiye wakusunsa pamodzi ndi Ine m'mbale.

Werengani mutu wathunthu Marko 14