Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 14:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paskha ndi mikate yopanda cotupitsa; ndipo ansembe akuru ndi alembi anafunafuna momcitira ciwembu, ndi kumupha:

2. pakuti anati, Paphwando ai, kuti pangakhale phokoso la anthu.

3. Ndipo pakukhala iye ku Betaniya m'nyumba ya Simoni wakhate, m'mene anaseama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa yaalabastero ya mafuta onunkhira bwino a nardo weni weni a mtengowapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pace.

4. Koma anakhalako ena anabvutika mtima mwa iwo okha, ndi kuti, Mafutawo atayidwa cifukwa ninji?

5. Pakuti mafuta amene akadagula marupiya atheka mazana atatu ndi mphambu zace, ndi kupatsa aumphawi. Ndipo anadandaulira mkaziyo.

6. Koma Yesu anati, Mlekeni, mumbvutiranji? wandicitira Ine nchito yabwino.

7. Pakuti muli nao aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo pali ponse pamene mukafuna mukhoza kuwacitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse.

8. Iye wacita cimene wakhoza; anandidzozeratu thupi langa ku kuikidwa m'manda.

9. Ndipo ndithu ndinena ndi inu, Ponse pamene padzalalikidwa Uthenga Wabwino ku dziko lonse lapansi, icinso cimene anacita mkazi uyu cidzanenedwa, cikhale comkumbukira naco.

10. Ndipo Yudase Isikariote, ndiye mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anacoka napita kwa ansembe akuru, kuti akampereke Iye kwa iwo.

Werengani mutu wathunthu Marko 14