Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 13:18-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo pempherani kuti kusakhale m'nyengo yacisanu.

19. Pakuti masiku aja padzakhala cisautso, conga sicinakhala cinzace kuyambira ciyambi ca cilengedwe cimene Mulungu anacilenga ndi kufikira tsopano, ndipo sicidzakhalanso nthawi zonse.

20. Ndipo Ambuye akadapanda kufupikitsa masikuwo, sakadapulumuka munthu mmodzi yense; koma cifukwa ca osankhidwa amene anawasankha, anafupikitsa masikuwo.

21. Ndipo pamenepo wina akati kwa inu, Onani Kristu ali pano; kapena, Onani, uko; musabvomereze;

22. pakuti adzauka Akristu onyenga ndi aneneri onyenga, ndipo adzacita zizindikilo ndi zozizwitsa, kuti akasoceretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe.

23. Koma yanganirani; onani ndakuuziranitu zinthu zonse, zisanafike.

24. Koma m'masikuwo, citatha cisautso cimeneco, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzapatsa kuunika kwace,

25. ndi nyenyezi zidzagwa kucokera m'mwamba ndi mphamvu ziri m'mwamba zidzagwedezeka.

26. Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa munthu alinkudza m'mitambo ndi mphamvu yaikuru, ndi ulemerero.

27. Ndipo pamenepo adzatuma angelo, nadzasonkhanitsa osankhidwa ace ocokera ku mphepo zinai, kuyambira ku malekezero ace a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo.

28. Ndipo phunzirani ndi mkuyu fanizo lace; pamene pafika kuti nthambi yace ikhala yanthete, ndipo anaphuka masamba ace, muzindikira kuti layandikira dzinja;

29. comweco inunso, pamene muona zinthu izi zirikucitika, zindikirani kuti ali pafupi pakhomo.

Werengani mutu wathunthu Marko 13