Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 12:41-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. Ndipo Iye anakhala pansi pandunji pa mosungiramo zopereka, napenya kuti khamu la anthu alikuponya ndalama mosungiramo; ndipo eni cuma ambiri anaponyamo zambiri.

42. Ndipo anadza mkazi wamasiye waumphawi, ndipo iye anaponyamo tindalama tiwiri tanng'ono tofa kakobiri kamodzi.

43. Ndipo anaitana ophunzira ace, nati kwa iwo, Ndithu ndinena ndi inu, Mkazi wamasiye amene waumphawi anaponya zambiri koposa onse akuponya mosungiramo:

44. pakuti anaponyamo onse mwa zocuruka zao; koma iye anaponya mwa kusowa kwace zonse anali nazo, inde moyo wace wonse.

Werengani mutu wathunthu Marko 12