Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 12:30-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. ndipouzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.

31. Laciwiri ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina lakuposa awa.

32. Ndipo mlembiyo anati kwa Iye, Cabwino, Mphunzitsi, mwanena zoona kuti ndiye mmodzi; ndipo palibe wina, koma Iye:

33. ndipo, kumkonda Iye ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mnzace monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa.

34. Ndipo palmona kuti anayankha ndi nzeru, Yesu anati kwa iye, Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo palibe munthu analimbanso mtima kwnfunsa Iye kanthu.

35. Ndipo Yesu pamene anaphunzitsa m'Kacisi, anayankha, nanena, Bwanji alembi anena kuti Kristu ndiye mwana wa Davide?

36. Davide mwini yekha anati mwa Mzimu Woyera, Ambuye anati kwa Ambuye wanga, Khala ku dzanja langa lamanja, kufikira ndiwaika adani ako popondapo mapazi ako.

37. Davide mwini yekha amchula Iye Ambuye; ndipo ali mwana wace bwanji? Ndipo anthu a makamuwo anakondwa kumva Iye.

38. Ndipo m'ciphunzitso cace ananena, Yang'anirani mupewe alembi, akufuna kuyendayenda obvala miinjiro, ndi kulankhulidwa pamisika,

39. ndi kukhala nayo mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamapwando:

40. amenewo alusira nyumba za akazi amasiye, napemphera monyenga mau ambiri; amenewa adzalandira kulanga koposa.

41. Ndipo Iye anakhala pansi pandunji pa mosungiramo zopereka, napenya kuti khamu la anthu alikuponya ndalama mosungiramo; ndipo eni cuma ambiri anaponyamo zambiri.

42. Ndipo anadza mkazi wamasiye waumphawi, ndipo iye anaponyamo tindalama tiwiri tanng'ono tofa kakobiri kamodzi.

Werengani mutu wathunthu Marko 12