Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 12:23-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Pakuuka adzakhala mkazi wa yani wa iwowa? Pakuti asanu ndi awiriwo adamuyesa mkazi wao.

24. Yesu ananena nao, Simusocera nanga mwa ici, popeza mulibe kudziwa malembo, kapena mphamvu yace ya Mulungu?

25. Pakuti pamene adzauka kwa akufa, sakwatira, kapena sakwatiwa; koma akhala ngati angelo a Kumwamba. Koma za akufa, kuti akauldtsidwa;

26. simunawerenga m'kalata wa Mose kodi, za Citsambaco, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine Ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?

27. Sali Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: musocera inu ndithu.

28. Ndipo anadza mmodzi wa alembi, namva iwo alikufunsana pamodzi, ndipo pakudziwa kuti anawayankha bwino, anamfunsa Iye, Lamulo la m'tsogolo la onse ndi liti?

29. Yesu anayankha, kuti, La m'tsogolo ndili, Mvera, Israyeli; Ambuye Mulungu wathu, Ambuye ndiye mmodzi;

30. ndipouzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.

31. Laciwiri ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina lakuposa awa.

32. Ndipo mlembiyo anati kwa Iye, Cabwino, Mphunzitsi, mwanena zoona kuti ndiye mmodzi; ndipo palibe wina, koma Iye:

33. ndipo, kumkonda Iye ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mnzace monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa.

Werengani mutu wathunthu Marko 12