Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 11:7-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo anabwera naye mwana wa buru kwa Yesu, naika zobvala zao pa iye, ndipo Iye anakhala pamenepo.

8. Ndimo ambiri anayala zobvala zao panjira; ndi ena zitsamba, anazidula m'minda.

9. Ndipo akutsogolera, ndi iwo akutsata, anapfuula, Hosana; Wolemekezeka Iye wakudza m'dzina la Ambuye:

10. Wolemekezeka Ufumu ulinkudza, wa atate wathu Davide; Hosana m'Kumwamba-mwamba.

11. Ndipo Iye analowa m'Yerusalemu, m'Kacisi; ndipo m'mene anaunguza zinthu zonse, popeza ndi madzulo, anaturuka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwoo.

12. Ndipo m'mawa mwace, ataturuka ku Betaniya, Iye anamva njala.

13. Ndipo anaona mkuyu kutali, uli ndi masamba; ndipo anadza Iye, kuti kapena akapezapo kanthu: ndipo m'mene anafikako anapeza palibe kanthu koma masamba okha; pakuti siinali nyengo yace ya nkhuyu.

Werengani mutu wathunthu Marko 11