Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 11:14-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo anayankha nanena ndi uwo, Munthu sadzadyanso zipatso zako nthawi zonse. Ndipo ophunzira ace anamva,

15. Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa m'Kacisi, nayamba kuturutsa akugulitsa ndi akugula malonda m'Kacisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando yaogulitsa nkhunda;

16. ndipo sanalola munthu ali yense kunyamula cotengera kupyola pakati pa Kacisi.

17. Ndipo anaphunzitsa, nanena nao, Sicilembedwa kodi, Nyumba yanga idzachedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? koma inu mwaiyesa phanga la acifwamba.

18. Ndipo ansembe akuru ndi alembi anamva, nafunafuna momuonongera Iye; pakuti anamuopa, cifukwa khamu lonse la anthu linazizwa ndi ciphunzitso cace.

19. Ndipo masiku onse madzulo anaturuka Iye m'mudzi.

20. Ndipo m'mene anapitapo m'mawa mwace, anaona kuti mkuyu uja unafota, kuyambira kumizu.

21. Ndipo Petro anakumbukila, nanena naye, Rabi, onani, wafota mkuyuwo munautemberera.

22. Ndipo Yesu anayankha nanena nao, Khulupirirani Mulungu,

23. Ndithu ndinena ndi inu, kuti, Munthu ali yense akanena ndi phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja; wosakayika mumtima mwace, koma adzakhulupirira kuti cimene acinena cicitidwa, adzakhala naco.

24. Cifukwa cace ndinena ndi inu, Zinthu ziri zonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.

25. Ndipo pamene muimirira ndi kupemphera, kholulukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali Kumwamba akhulolukire inu zolakwa zanu.

27. Ndipo iwo anadzanso ku Yerusalemu; ndipo m'mene Iye anali kuyenda m'Kacisi, anafika kwa Iye ansembe akuru, ndi alembi ndi akuru;

28. nanena naye, Izi muzicita ndi ulamuliro wotani? Kapena anakupatsani ndani ulamuliro uwu wakucita izi?

29. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani mau amodzi, mundiyankhe Ine, ndipo ndidzakuuzani ulamuliro umene ndicita nao zinthu zimenezi.

Werengani mutu wathunthu Marko 11