Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 11:13-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo anaona mkuyu kutali, uli ndi masamba; ndipo anadza Iye, kuti kapena akapezapo kanthu: ndipo m'mene anafikako anapeza palibe kanthu koma masamba okha; pakuti siinali nyengo yace ya nkhuyu.

14. Ndipo anayankha nanena ndi uwo, Munthu sadzadyanso zipatso zako nthawi zonse. Ndipo ophunzira ace anamva,

15. Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa m'Kacisi, nayamba kuturutsa akugulitsa ndi akugula malonda m'Kacisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando yaogulitsa nkhunda;

16. ndipo sanalola munthu ali yense kunyamula cotengera kupyola pakati pa Kacisi.

17. Ndipo anaphunzitsa, nanena nao, Sicilembedwa kodi, Nyumba yanga idzachedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? koma inu mwaiyesa phanga la acifwamba.

18. Ndipo ansembe akuru ndi alembi anamva, nafunafuna momuonongera Iye; pakuti anamuopa, cifukwa khamu lonse la anthu linazizwa ndi ciphunzitso cace.

19. Ndipo masiku onse madzulo anaturuka Iye m'mudzi.

20. Ndipo m'mene anapitapo m'mawa mwace, anaona kuti mkuyu uja unafota, kuyambira kumizu.

21. Ndipo Petro anakumbukila, nanena naye, Rabi, onani, wafota mkuyuwo munautemberera.

22. Ndipo Yesu anayankha nanena nao, Khulupirirani Mulungu,

Werengani mutu wathunthu Marko 11