Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 11:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo m'mawa mwace, ataturuka ku Betaniya, Iye anamva njala.

13. Ndipo anaona mkuyu kutali, uli ndi masamba; ndipo anadza Iye, kuti kapena akapezapo kanthu: ndipo m'mene anafikako anapeza palibe kanthu koma masamba okha; pakuti siinali nyengo yace ya nkhuyu.

14. Ndipo anayankha nanena ndi uwo, Munthu sadzadyanso zipatso zako nthawi zonse. Ndipo ophunzira ace anamva,

15. Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa m'Kacisi, nayamba kuturutsa akugulitsa ndi akugula malonda m'Kacisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando yaogulitsa nkhunda;

16. ndipo sanalola munthu ali yense kunyamula cotengera kupyola pakati pa Kacisi.

17. Ndipo anaphunzitsa, nanena nao, Sicilembedwa kodi, Nyumba yanga idzachedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? koma inu mwaiyesa phanga la acifwamba.

18. Ndipo ansembe akuru ndi alembi anamva, nafunafuna momuonongera Iye; pakuti anamuopa, cifukwa khamu lonse la anthu linazizwa ndi ciphunzitso cace.

19. Ndipo masiku onse madzulo anaturuka Iye m'mudzi.

Werengani mutu wathunthu Marko 11