Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 11:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri la Azitona, anatuma awiri a ophunzira ace,

2. nanena nao, Mukani, lowani m'mudzi wapandunji ndi inu; ndipo pomwepo pakulowamo mudzapeza mwana wa buru womangidwa, amene palibe munthu anakhalapo kale lonse; mmasuleni, ndipo mubwere naye.

3. Ndipo munthu akati kwa inu, Mutero bwanji? Katini, Ambuye amfuna iye; ndipo pomwepo adzamtumiza kuno.

4. Ndipo anacoka, napeza mwana wa buru womangidwa pakhomo, pabwalo m'khwalala, nammasula iye.

5. Ndipo ena akuima kumeneko ananena nao, Mucita ciani ndi kumasula mwana wa buru?

6. Ndipo anati kwa iwo monga momwe ananena Yesu: ndipo anawalola iwo apite naye.

7. Ndipo anabwera naye mwana wa buru kwa Yesu, naika zobvala zao pa iye, ndipo Iye anakhala pamenepo.

8. Ndimo ambiri anayala zobvala zao panjira; ndi ena zitsamba, anazidula m'minda.

9. Ndipo akutsogolera, ndi iwo akutsata, anapfuula, Hosana; Wolemekezeka Iye wakudza m'dzina la Ambuye:

10. Wolemekezeka Ufumu ulinkudza, wa atate wathu Davide; Hosana m'Kumwamba-mwamba.

11. Ndipo Iye analowa m'Yerusalemu, m'Kacisi; ndipo m'mene anaunguza zinthu zonse, popeza ndi madzulo, anaturuka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwoo.

12. Ndipo m'mawa mwace, ataturuka ku Betaniya, Iye anamva njala.

Werengani mutu wathunthu Marko 11