Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 10:9-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Cifukwa cace cimene Mulungu anacimanga pamodzi, asacilekanitse munthu.

10. Ndipo m'nyumba ophunzira anamfunsanso za cinthu ici.

11. Ndipo Iye ananena nao, Munthu ali yense akacotsa mkazi wace, nakakwatira wina, acita cigololo kulakwira mkaziyo;

12. ndipo ngati mkazi akacotsa mwamuna wace, nakwatiwa ndi wina, acita cigololo iyeyu.

13. Ndipo analinkudza nato kwa Iye tiana, kuti akatikhudze; ndipo ophunzirawo anawadzudzula.

14. Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.

15. Ndithu ndinena ndi inu, Munthu ali yense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse.

16. Ndipo Iye anatiyangata, natidalitsa, ndi kuika manja ace pa ito.

17. Ndipo pamene Iye anaturuka kutsata njira, anamthamangira munthu, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndidzacita ciani kuti ndilandire moyo wosatha?

Werengani mutu wathunthu Marko 10