Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 10:3-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo Iye anayankha nati kwa iwo, Kodi Mose anakulamulirani ciani?

4. Ndipo anati, Mose analola kulembera kalata wakulekanira, ndi kumcotsa.

5. Koma Yesu anati kwa iwo, Cifukwa ca kuuma kwa mitima yanu anakulemberani lamulo ili.

6. Koma kuyambira pa ciyambi ca malengedwe anawapanga mwamuna ndi mkazi.

7. Cifukwa cace mwamuna adzasiya atate wace ndi amai wace, ndipo adzaphatikizana ndi mkazi wace;

8. ndipo awiriwa adzakhala thupi limodzi: kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi.

9. Cifukwa cace cimene Mulungu anacimanga pamodzi, asacilekanitse munthu.

10. Ndipo m'nyumba ophunzira anamfunsanso za cinthu ici.

11. Ndipo Iye ananena nao, Munthu ali yense akacotsa mkazi wace, nakakwatira wina, acita cigololo kulakwira mkaziyo;

12. ndipo ngati mkazi akacotsa mwamuna wace, nakwatiwa ndi wina, acita cigololo iyeyu.

13. Ndipo analinkudza nato kwa Iye tiana, kuti akatikhudze; ndipo ophunzirawo anawadzudzula.

14. Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.

15. Ndithu ndinena ndi inu, Munthu ali yense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse.

16. Ndipo Iye anatiyangata, natidalitsa, ndi kuika manja ace pa ito.

Werengani mutu wathunthu Marko 10