Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 10:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ananyamuka Iye kumeneko, nadza ku maiko a ku Yudeya ndi ku tsidya lija la Yordano; ndipo anasonkhananso kwa Iye makamu a anthu; ndipo monga anazolowera, anawaphunzitsanso.

2. Ndipo anadza kwa Iye Afarisi, namfunsa Iye ngati kuloledwa kuti munthu acotse mkazi wace, namuyesa Iye.

3. Ndipo Iye anayankha nati kwa iwo, Kodi Mose anakulamulirani ciani?

Werengani mutu wathunthu Marko 10