Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 1:8-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndakubatizani inu ndi madzi; koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.

9. Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kucokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane m'Yordano.

10. Ndipo pomwepo, alimkukwera poturuka m'madzi, anaona Iye thambo litang'ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda:

11. ndipo mau anaturuka m'thambo, Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino.

12. Ndipo pomwepo Mzimu anamkangamiza kunka kucipululu.

13. Ndipo anakhala m'cipululu masiku makumi anai woyesedwa ndi Satana; nakhala ndi zirombo, ndipo angelo anamtumikira.

14. Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira uthenga wabwino wa Mulungu,

15. nanena, Nthawi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani uthenga wabwino.

16. Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andreya, mbale wace wa Simoni, alinkuponya psasa m'nyanja; pakuti anali asodzi.

17. Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu.

18. Ndipo pomwepo anasiya makoka ao, namtsata Iye.

Werengani mutu wathunthu Marko 1