Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 1:34-45 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. Ndipo anaciritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundu mitundu, naturutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalola ziwandazo zilankhule, cifukwa zinamdziwa Iye.

35. Ndipo m'mawa mwace anauka usikusiku, naturuka namuka kucipululu, napemphera kumeneko.

36. Ndipo Simoni ndi anzace anali naye anamtsata,

37. nampeza, nanena naye, Akufunani inu anthu onse.

38. Ndipo ananena nao, Tiyeni kwina, ku midzi iri pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera nchito imene.

39. Ndipo analowa m'masunagoge mwao m'Galileya monse, nalalikira, naturutsa ziwanda.

40. Ndipo anadza kwa Iye wodwala khate, nampempha Iye, namgwadira, ndi kunena ndi Iye, Ngati mufuna mukhoza kundikonza.

41. Ndipo Yesu anagwidwa cifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa.

42. Ndipo pomwepo khate linamcoka, ndipo anakonzedwa.

43. Ndipo anamuuzitsa, namturutsa pomwepo,

44. nanena naye, Ona, usati unene kanthu kwa munthu ali yense: koma muka, ukadzionetse kwa wansembe, nupereke pa makonzedwe ako 1 zimene adalamulira Mose, zikhale mboni kwa iwo.

45. Koma 2 iye anaturuka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanadziwa kulowansopoyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a ku malo onse.

Werengani mutu wathunthu Marko 1