Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 1:31-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. ndipo anadza namgwira dzanja, namuutsa; ndipo malungo anamleka, ndipo anawatumikira iwo.

32. Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nao kwa Iye onse akudwala, ndi akugwidwa ndi ziwanda.

33. Ndipo mudzi wonse unasonkhana pakhomo.

34. Ndipo anaciritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundu mitundu, naturutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalola ziwandazo zilankhule, cifukwa zinamdziwa Iye.

35. Ndipo m'mawa mwace anauka usikusiku, naturuka namuka kucipululu, napemphera kumeneko.

36. Ndipo Simoni ndi anzace anali naye anamtsata,

37. nampeza, nanena naye, Akufunani inu anthu onse.

38. Ndipo ananena nao, Tiyeni kwina, ku midzi iri pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera nchito imene.

Werengani mutu wathunthu Marko 1