Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 1:19-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo atapita patsogolo pang'ono, anaona Yakobo, mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace, iwonso anali m'combo nakonza makoka ao.

20. Ndipo pomwepo anawaitana: ndipo anasiya atate wao Zebedayo m'combomo pamodzi ndi anchito olembedwa, namtsata.

21. Ndipo iwo analowa m'Kapemao; ndipo pomwepo pa dzuwa la Sabata iye analowa m'sunagoge naphunzitsa,

22. Ndipo anazizwa ndi ciphunzitso cace; pakuti anaphunzitsa monga mwini mphamvu, si monga alembi.

23. Ndipo pomwepo panali munthu m'sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anapfuula iye

24. kuti, Tiri ndi ciani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife? Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu.

25. Ndipo Yesu anaudzudzula, kuti, Khala uli cete, nuturuke mwa iye.

26. Ndipo mzimu wonyansa, pomng'amba, ndi kupfuula ndi mau akuru, unaturuka mwa iye.

27. Ndipo anazizwa onse, kotero kuti anafunsana mwa iwo okha, kuti, Ici nciani? ciphunzitso catsopano! ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imvera Iye.

28. Ndipo mbiri yace inabuka pompaja ku dziko lonse la Galileya lozungulirapo.

29. Ndipo pomwepo, poturuka m'sunagoge, iwo analowa m'nyumba ya Simoni ndi Andreya pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane,

30. Ndipo mpongozi wace wa Simoni anali gone wodwala malungo; ndipo pomwepo anamuuza za iye:

31. ndipo anadza namgwira dzanja, namuutsa; ndipo malungo anamleka, ndipo anawatumikira iwo.

32. Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nao kwa Iye onse akudwala, ndi akugwidwa ndi ziwanda.

33. Ndipo mudzi wonse unasonkhana pakhomo.

Werengani mutu wathunthu Marko 1