Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 1:14-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira uthenga wabwino wa Mulungu,

15. nanena, Nthawi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani uthenga wabwino.

16. Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andreya, mbale wace wa Simoni, alinkuponya psasa m'nyanja; pakuti anali asodzi.

17. Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu.

18. Ndipo pomwepo anasiya makoka ao, namtsata Iye.

19. Ndipo atapita patsogolo pang'ono, anaona Yakobo, mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace, iwonso anali m'combo nakonza makoka ao.

20. Ndipo pomwepo anawaitana: ndipo anasiya atate wao Zebedayo m'combomo pamodzi ndi anchito olembedwa, namtsata.

21. Ndipo iwo analowa m'Kapemao; ndipo pomwepo pa dzuwa la Sabata iye analowa m'sunagoge naphunzitsa,

22. Ndipo anazizwa ndi ciphunzitso cace; pakuti anaphunzitsa monga mwini mphamvu, si monga alembi.

Werengani mutu wathunthu Marko 1