Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 1:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. CIYAMBI cace ca Uthenga Wabwino wa Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu.

2. Monga mwalembedwa m'Yesaya mneneri,Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu,Amene adzakonza njira yanu;

3. Mau a wopfuula m'cipululu, Konzani khwalala la Ambuye, Lungamitsani njira zace;

4. Yohane anadza nabatiza m'cipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku cikhululukiro ca macimo.

5. Ndipo anaturuka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordano, poulula macimo ao.

6. Ndipo Yohane anabvala ubweya wa ngamila, ndi lamba lacikopa m'cuuno mwace, nadya dzombe ndi uci wa kuthengo.

7. Ndipo analalikira, kuti, Wondipambana ine mphamvu akudza pambuyo panga, sindiyenera kuwerama kumasula lamba la nsapato zace ine.

Werengani mutu wathunthu Marko 1