Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 9:5-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Koma anati, Ndiouyani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;

6. komatu, uka, nulowe m'mudzi, ndipo kudzanenedwa kwa iwe cimene uyenera kucita.

7. Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima du, atamvadi mau, koma osaona munthu.

8. Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ace, sanapenya kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye ni'Damasiko.

9. Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadya kapena kumwa.

10. Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lace Hananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Hananiya. Ndipo anati, Ndiri pano, Ambuye,

11. Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lochedwa Lolunjika, ndipo m'nyumba ya Yuda ufunse za munthu dzina lace Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera

12. ndipo anaona mwamuna dzina, lace Hananiya, alikulowa, namuika manja, kuti apenyenso.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 9