Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 9:29-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. nanena molimbika mtima m'dzina la Ambuye; ndipotu analankhula natsutsana ndi Aheleniste; koma anayesayesa kumupha iye.

30. Koma m'mene abale anacidziwa, anapita naye ku Kaisareya, namtumiza acokeko kunka ku Tariso.

31. Pamenepo ndipo Mpingo wa m'Yudeya Ionse ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'citonthozo ca Mzimu Woyera, nucuruka.

32. Koma kunali, pakupita Petro ponse ponse, anatsikiranso kwa oyera mtima akukhalaku Luda.

33. Ndipo anapeza kumeneko munthu dzina lace Eneya, amene anagonera pamphasa zaka zisanu ndi zitatu; amene anagwidwa manjenje.

34. Ndipo Petro anati kwa iye, Eneya, Yesu Kristu akuciritsa iwe; uka, yalula mphasa yako. Ndipo anauka pomwepo.

35. Ndipo anamuona iye onse akukhala ku Luda ndi ku Sarona, natembenukira kwa Ambuye amenewa.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 9