Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 9:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma Saulo, wosaleka kupumira pa akuphunzira a Ambuye kuopsya ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe,

2. napempha kwa iye akalata akunka nao ku Damasiko kumasunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.

3. Ndipo poyenda ulendo wace, kunali kuti iye anayandikira Damasiko: ndipo mwadzidzidzi kudawala momzingira kuunika kocokera kumwamba;

4. ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?

5. Koma anati, Ndiouyani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;

6. komatu, uka, nulowe m'mudzi, ndipo kudzanenedwa kwa iwe cimene uyenera kucita.

7. Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima du, atamvadi mau, koma osaona munthu.

8. Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ace, sanapenya kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye ni'Damasiko.

9. Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadya kapena kumwa.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 9