Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 8:32-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Koma palembo pamene analikuwerengapo ndipo.Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa,Ndi monga mwana wa nkhosa ali du pamaso pa womsenga,Kotero sanatsegula pakamwa pace:

33. M'kucepetsedwa kwace ciweruzo cace cinacotsedwa;Mbadwo wace adzaubukitsa ndani?Cifukwa wacotsedwa kudziko moyo wace.

34. Ndipo mdindoyo anayankha Filipo, nati, Ndikupempha, mneneri anena ici za yani? za yekha, kapena za wina?

35. Ndipo Filipo anatsegula pakamwa pace, nayamba pa lembo ili, nalalikira kwa iye Yesu.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 8