Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 8:31-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Koma anati, Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine? ndipo anapempha Filipo akwere nakhale naye.

32. Koma palembo pamene analikuwerengapo ndipo.Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa,Ndi monga mwana wa nkhosa ali du pamaso pa womsenga,Kotero sanatsegula pakamwa pace:

33. M'kucepetsedwa kwace ciweruzo cace cinacotsedwa;Mbadwo wace adzaubukitsa ndani?Cifukwa wacotsedwa kudziko moyo wace.

34. Ndipo mdindoyo anayankha Filipo, nati, Ndikupempha, mneneri anena ici za yani? za yekha, kapena za wina?

35. Ndipo Filipo anatsegula pakamwa pace, nayamba pa lembo ili, nalalikira kwa iye Yesu.

36. Ndipo monga anapita paniire pao, anadza ku madzi akuti; ndipo mdindoyo anati, Taonapo madzi; cindiletsa ine ciani ndisabatizidwe? [

37. ]

38. Ndipo anamuuza kuti aimitse gareta; ndipo anatsikira onse awiri kumadzi, Filipo ndi mdindoyo; ndipoanambatiza iye.

39. Ndipo pamene anakwera kururuka m'madzi, Mzimu wa Ambuye anakwatula Filipo; ndipo mdindo sanamuonanso, pakuti anapita njira yace wokondwera.

40. Koma Filipo anapezedwa ku Azotu; ndipo popitapitaanalalikira Uthenga Wabwino m'midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kaisareya.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 8