Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 8:12-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwinowa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Kristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.

13. Ndipo Simoni mwini wace anakhulupiranso: ndipo m'mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikilo ndi mphamvu zazikuru zirikucitika, anadabwa.

14. Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane;

15. amenewo, m'mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera:

16. pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwam'dzina la Ambuye Yesu.

17. Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.

18. Koma pakuona Simoni kuti mwa kuika manja a atumwi anapatsidwa Mzimu Woyera, anawatengera ndalama,

19. nanena, Ndipatseni inenso ulamuliro umene, kuti amene ali yense ndikaika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera.

20. Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, cifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama.

21. Ulibe gawo kapena colandira ndi mau awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu.

22. Cifukwa: cace lapa coipa calm ici, pemphera Ambuye, kuti kapena akukhululukire iwe colingiriraca mtima wako.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 8