Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 7:49-60 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

49. 21 Thambo la kumwamba ndilo mpando wacifumu wanga,Ndi dziko lapansi copondapo mapazi anga:Mudzandimangira nyumba yotani? ati Ambuye;Kapena malo a mpumulo wanga ndi otani?

50. Silinapanga dzanja langa zinthu izi zonse kodi?

51. 22 Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anacita makolo anu, momwemo inu.

52. 23 ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunza? ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudzakwace kwa Wolungamayo; wa iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;

53. inu amene munalandira cilamulo 24 monga cidaikidwa ndi angelo, ndipo simunacisunga.

54. Koma pakumva izi analaswa mtima, namkukutira mano.

55. Koma iye, 25 pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu,

56. nati, Taonani, 26 ndipenya m'Mwamba motseguka, ndi Mwana wa munthu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu.

57. Koma anapfuula ndi mau akuru, natseka m'makutu mwao, namgumukira iye ndi mtima umodzi;

58. ndipo 27 anamtaya kunja kwa mudzi, namponya miyala; ndipo 28 mbonizo zinaika zobvala zao pa mapazi a mnyamata dzina lace Saulo.

59. Ndipo anamponya miyala Stefano, alikuitana Ambuye, ndi kunena, 29 Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.

60. Ndipo m'mene anagwada pansi, anapfuula ndi mau akuru, 30 Ambuye, musawaikire iwo cimo ili. Ndipo m'mene adanena ici, anagona tulo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 7